PEMPHERO LA AHMAD (#13478)

Iye Ndiye Mfumu, Wodziwa zonse, Wanzeru! 
Taonani, Mbalame ya M’Paradiso iyimba pa nthambi za Mtengo Wamuyaya, ndi nyimbo zoyera ndi zokoma, kulalikira kwa woona mtima thenga wabwino wa kuyandikira kwa Mulungu kuwaitanira okhulupilira mu Umodzi wa Uzimu kubwalo la Pamaso pa Wopatsayo, kuwauza anthu wotsatira za uthenga womwe wabvumbulutsidwa ndi Mulungu, Mfumu, Waulemerero, Wopanda mzake, kuwatsogolera okondedwa kumpando wopatulika ndi kwa wokongola konyezimirayu.  
Indetu, Uyu ndi Wokongola Kopambana amene ananenedwa m’mabukhu a Atumwi, kupyolera mwa amene choonadi chidzalekanitsidwa ndi chonama ndipo nzeru ya lamulo lirilonse idzayesedwa. Indetu, Iye Ndiye Mtengo wa Moyo umene umabweretsa zipatso za Mulungu, Wokwezeka, Wamphamvu, Wamkulu.  
O Ahmad! Chitirani umboni kuti ndithudi Iye Ndiye Mulungu ndipo palibe Mulungu koma Iye, Mfumu, Mtetezi, Wosafanizidwa, Mwini Mphamvu. Amene Iye 
Wamtuma m’dzina loti Ali (Bábu Woyera) anali Woona wodzera kwa Mulungu Amene Malamulo Ake tonse tibvomereza.  
Nenani: O wanthu inu khalani omvera malangizo a Mulungu amene alembedwa mu Bayani ndi wa Ulemereloyo, Wanzeru. Ndithudi, Iye ndi Mfumu ya Atumwi ndipo Bukhu Lake ndi Mai wa Mabukhu mukadadziwa.  
Chomwecho Mbalame ikuitana inu kuchokera mu ndende iyi. Iye Ayenera kupereka uthenga womvekawu. Kwa iye amene safuna aukane uphunguwu ndi kwa iye amene afuna asankhe njira yopita kwa Ambuye ake. O anthu inu, ngati mukana mau awa, mwakhulupilira mwa Mulungu ndi chitsimikizo chotani? Tiwonetseni, O gulu la wabodza. Ai, mwa M’modzi Amene asunga moyo wanga m’dzanja Lake sangathe ndipo sadzatha kuchita izi ngakhale atagwirizana kuthandizana wina ndi mzake.  
O Ahmad! Musaiwale mphatso Zanga pamene Ine palibe. 
Kumbukirani masiku Anga m’masiku a moyo wanu ndi masautso Anga ndi kumangidwa Kwanga m’ndende iyi yakutali. Ndipo khalani wolimbika m’chikondi Changa kuti mtima wanu usagwedezeke, ngakhale malupanga a adani akukang’antheni ndi kumwamba konse ndi dziko zikuukileni. Khalani monga lawi la moto kwa adani Anga ndi mtsinje wa moyo wosatha kwa wokondedwa Anga, ndipo musakhale a iwo wokaika. Ndipo mukakumana ndi zosautsa m’njira Yanga kapena kunyazitsidwa chifukwa cha Ine, musabvutike nazo.  
Tsamilani pa Mulungu, Mulungu wanu ndi Ambuye wa atate anu. Chifukwa anthu akusokera m’njira za chitaiko, osatha kuona Mulungu ndi maso awo, kapena kumva nyimbo Yake ndi makutu awo. Ndi momwe Tawapezera, monga nanunso muchitira umboni. Ndichifukwa chake miyambo yao yosanduka zophimba pakati pa iwo ndi mitima yao ndikuwachotsa iwo m’njira ya Mulungu, Wokwezeka, Wamkulu.  
Muyenera kutsimikiza mwa inu nokha kuti ndithudi, iye amene samvera Wokongolayu wakananso kumvera Atumwi onse akale ndipo wasonyeza kunyada pamaso pa Mulungu kuyambira ku nthawi zosayamba mpaka ku nthawi zosatha.  
Phunzirani bwino pemphero ili, O Ahmad. Lineneni m’masiku anu ndipo musadzilekelere nokha m’menemo. Pakuti ndithudi, Mulungu wamukonzera iye wakulinena mphoto ya ophedwa oyera mtima zana limodzi ndi kumtumikira m’maiko onse awiri. Zaulerezi Tazipereka kwa inu ngati mtulo ku mbali Yathu ndi chifundo chodzera ku malo Athu, kuti mukhale a iwo woyamika.  
Pali Mulungu! Ngati wina ali m’zowawa kapena m’chisoni nawerenga Pempheroli ndi mtima wonse, Mulungu Adzakankha chisoni chake, nakonza zobvuta zake ndi kuchotsa zowawa zake. Ndithudi, Iye ndi Wachifundo, Wachisoni. Mayamiko akhale kwa Mulungu, Ambuye wa maiko onse.

-Bahá'u'lláh
-----------------------

